Steven Fulakeza

Ndinakachedza kumadera adziko la Liberia tsiku lachiwiri ndipo ndinali odzizwa. Tinalipo asanu aife omwe tinakhala kutsogolo kwa minibasi. Awiri adakhala apo pamene ayenera kukhala oyendetsa, ena awiri adakhala pokhala okwera modzi, ndipo wina m’modzi wachisanuyo anadzithithikidza pa giya. Munthu wabambo yemwe anali kumanja kwanga ankandithithikiza moyipa. Ndidali wokwiya komanso thupi lonse ndidali fumbi lokhalokha. Kuphatikiza apo buluku lomwe ndidavala lidamatidwa ndi ndowe dza  munthu dzomwe ndidaponda munseu.

Titayenda kwa maola asanu tidafika komwe timapita koma nditatopa ndi kulimba ndi bambo wantopolayo. Pofika adandipansa kansalu kuti ndidzipukutire kumanso fumbi ndidadzola njiralo. Panthawiyi ndikuti tikudikira kuti tiyambe mwambo omwe tidapitira uku. Wina adafunsa kuti ndi pukutenso tsitsi lomwe lidafira ndi fumbinso. Atsika ndikati ndikuuzene…Field Research simachedza.

Adanditengera ku malo kokhala anthu othawa mabvuto kwawo komwe ndidakuma ndi amayi achi Liberia osiyanasiyana. Ndinali odabwa ndi nkhani dzawo. Ena mwa iwo ankati “ndidagwiriridwa ndi amuna asanu…ndimatuluka magazi nthawi iliyonseyo ndikagonana ndi mamuna”. Ndi ndimangoti chabwino achemwali..pepani…zikomo achemwali. Uku tikuyendabe kukumana ndi amayi ena.

Modzi mwa imayiywo anayankhula nane momvetsa chisino nati, ndiwe mwana wanga ndipo ndine mayi wako. Mwana wanga satha kuwerenga. Adapitiridza modandaula.

Padalibe china chomwe ndikadapanga koma kumangolira.